Awoneseni - Ricco Dee

Awoneseni - Ricco Dee
Awoneseni - Ricco Dee
From the album Unlimited the Mixtape

Song Lyrics

Intro:

Stoical Firm, Stoical!
Heeey
Niekay,
Eh, Achina Forces

Young D on this one

Verse1 (Young D)
Ambuye alinafe nthawi zonse nyengo zonse
Mumatisamalila ndingapite kulikonse
Munalenga kumwamba, dziko nchina chilichonse
Ngakhale ena amaphweketsa china chilichonse
Awoneseni adziwe ukulu wanu
Misodzi ingotsika sadziwa ukulu wanu
Ndili ndi moyo kamba Ka chikondi Chanu
Chilichonse ndi chanu palibe ofana nanu
Satana!
Alibe mphamvu amachepera
Mavuto kundiliza mumati mwana sendera
Mu dzina lanu zikatheka ati ntera
Kutsatila uchimo ngati khini ya kulera
Kutengeka ndi dziko, lusifala ndamukana
Kulibwino ndikhale kape ndikumazimana
Dziko lavuta nkhondo, anthu angophana
Awoneseni ukulu wanu ndikupempha bwana

Hook (Niekay)
Yeah,
Awonetseleni, ukulu wanu
(ukulu wanu)
Awoneseleni, mphamvu zanu
(Mphamvu zanu)
Akuphweketsa, akudelera iwooo/
Akuyetsa ndinu size yawo
Akuphweketsa, akudelera iwooo/
Akuyetsa ndinu size yawo

Verse 2 (Achina Forces)
(Achina Forces)
Anthuwa sakudziwa ndani Ali mbali yanga
Ambuye wakumwamba amadziwa dzina langa
Angolubwalubwa anthuwa alibe data
Ndimayenda ndi Yesu, ndi Yesuyo ndi Ma Deta
Kungowadziwitsa kuti ayenera adziwe
Kuti chitsime cha moyo, Yesuyo ndi langa dziwe
Kusosola gele ndikudzasosola beat
Munyengo yozizila ndidzatulutsa hit
Nkupangitsa kuti, wina apange quit
Zimene amapangazo nkuyamba kupemphera
Umangodziwiratu, Wa Yesu sachepera
Team yosapepela, chomwe amalephera Yesuyo ndi Kulephera
Chouluka chosatela
Kuuponya mu ukonde osaponyera padela
Eya, osapempherayo azipsa mtima adh a
Eeh, Kuning'ina adha

Hook (Niekay)
Yeah,
Awonetseleni, ukulu wanu
(ukulu wanu)
Awoneseleni, mphamvu zanu
(Mphamvu zanu)
Akuphweketsa, akudelera iwooo/
Akuyetsa ndinu size yawo
Akuphweketsa, akudelera iwooo/
Akuyetsa ndinu size yawo

Verse 3
(Niekay)
Akutamika, akusamalika
Akuyesa mwagona, kuti mwina simukuona
Mbuye zioneseleni
Manyaziwa nchotseleni
Adziwe kuti ndinu Ambuye
Mbuye zioneseleni
Manyaziwa nchotseleni
Adziwe kuti ndinu Ambuyeeeee eeehh

(Forces)
Sodom ndi Gomola munatentha
Bala munamuonetsa Sheba
Pharaoh anazionela yekha, mpaka Ana anu munatenga
Jah, awoneseni kuti ndinu consuming fire
Mavuto angachuluke ine simunditaya
Awoneseni kuti ndinu mwini dziko
Mudziko lanulo ineyo ndine nzika

Hook (Niekay)
Yeah,
Awonetseleni, ukulu wanu
(ukulu wanu)
Awoneseleni, mphamvu zanu
(Mphamvu zanu)
Akuphweketsa, akudelera iwooo/
Akuyetsa ndinu size yawo
Akuphweketsa, akudelera iwooo/
Akuyetsa ndinu size yawo
X2

Outro
Akuphweketsaa aaaaah